Masalmo 33:10-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Yehova aphwanya upo wa amitundu:Asandutsa cabe zolingirira za mitundu ya anthu.

11. Ciweruzo ca Yehova cikhazikika cikhazikikire,Zolingirira za m'mtima mwace ku mibadwo mibadwo.

12. Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao;Mtundu womwe anausankha ukhale colandira ca iye yekha.

13. Yehova apenyerera m'mwamba; Aona ana onse a anthu.

Masalmo 33