3. Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,Mtima wanga sungacite mantha:Ingakhale nkhondo ikandiukira,Nde pomweponso ndidzakhulupira,
4. Cinthu cimodzi ndinacipempha kwa Yehova, ndidzacilondola ici:Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,Kupenya kukongola kwace kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kacisi wace.
5. Cifukwa kuti pa dzuwa la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwace:Adzandibisa m'tsenjezi mwa cihema cace;Pathanthwe adzandikweza.
6. Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga;Ndipo ndidzapereka m'cihema mwace nsembe za kupfuula mokondwera;Ndidzayimba, inde, ndidzayimbira Yehova zomlemekeza.
7. Imvani, Yehova, liu langa popfuula ine:Mundicitirenso cifundo ndipo mundibvomereze.