Masalmo 24:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zace zomwe,Dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.

2. Pakuti Iye analimanga pazinyanja,Nalikhazika pamadzi.

3. Adzakwera ndani m'phiri la Yehova?Nadzaima m'malo ace oyera ndani?

4. Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye;Iye amene sanakweza moyo wace kutsata zacabe,Ndipo salumbira monyenga,

Masalmo 24