Masalmo 21:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti mumuikira madalitso ku nthawi zonse;Mumkondweretsa ndi cimwemwe pankhope panu.

7. Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,Ndipo mwa cifundo ca Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye,

8. Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse:Dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.

9. Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.Yehova adzawatha m'kukwiya kwace,Ndipo moto udzawanyeketsa.

Masalmo 21