Masalmo 19:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu;Ndipo thambo lionetsa nchito ya manja ace.

2. Usana ndi usana ucurukitsa mau,Ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.

3. Palibe cilankhulidwe, palibe mau;Liu lao silimveka.

4. Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi,Ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu.Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,

5. Ndipo liri ngati mkwati wakuturuka m'cipinda mwace,Likondwera ngati ciphona kuthamanga m'njira.

Masalmo 19