Masalmo 18:25-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Pa wacifundo mukhala wacifundoPa mumthu wangwiro mukhala wangwiro;

26. Pa woyera mtima mukhala woyera mtima;Pa wotsutsatsutsa mukhala wotsutsana naye.

27. Pakuti Inu muwapulumutsa anthu aumphawi;Koma maso okweza muwatsitsa.

28. Pakuti Inu muyatsa nyali yanga;Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

29. Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu;Ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga.

30. Mulungu ndiyewangwiro m'njira zace;Mau a Yehova ngoyengeka; Ndiye cikopa ca onse okhulupirira Iye.

31. Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova?Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu?

32. Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m'cuuno,Nakonza njira yanga ikhale yangwiro.

Masalmo 18