1. Yehova, ndani adzagonera m'cihema mwanu?Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika?
2. Iye wakuyendayo mokwanira, nacita cilungamo,Nanena zoonadi mumtima mwace.
3. Amene sasinjirira ndi lilime lace,Sacitira mnzace coipa,Ndipo satola msece pa mnansi wace.