Masalmo 142:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipfuula nalo liu langa kwa Yehova;Ndi mau anga ndipemba kwa Yehova.

2. Nditsanulirakudandaulakwanga pamaso pace;Ndionetsa msauko wanga pamaso pace.

3. Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga.M'njira ndiyendamo anandichera msampha,

4. Penyani ku dzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa;Pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.

Masalmo 142