Masalmo 141:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine;Mundicherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.

2. Pempherolanga liikike ngaticofukiza pamaso panu;Kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.

3. Muike mdindo pakamwa panga, Yehova;Sungani pakhomo pa milomo yanga.

4. Mtima wanga usalinge ku cinthu coipa,Kucita nchito zoipaNdi anthu akucita zopanda pace;Ndipo ndisadye zankhuli zao.

Masalmo 141