Masalmo 137:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ku mitsinje ya ku Babulo,Kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira,Pokumbukila Ziyoni.

2. Pa msondodzi uli m'mwemo Tinapacika mazeze athu.

3. Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo,Ndipo akutizunza anafuna tisekere,Ndi kuti, Mutiyimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.

4. Tidati, Tidzayimba bwanji nyimbo ya YehovaM'dziko lacilendo?

Masalmo 137