Masalmo 135:6-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ciri conse cimkonda Yehova acicita,Kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse.

7. Akweza mitambo icokere ku malekezero a dziko lapansi;Ang'animitsa mphezi zidzetse mvula;Aturutsa mphepo mosungira mwace.

8. Anapanda oyamba a Aigupto,Kuyambira munthu kufikira zoweta.

9. Anatumiza zizindikilo ndi zodabwiza pakati pako,Aigupto iwe, Pa Farao ndi pa omtumikira onse.

10. Ndiye amene anapanda amitundu ambiri.Napha mafumu amphamvu;

11. Sihoni mfumu ya Aamori,Ndi Ogi mfumu ya Basana,Ndi maufumu onse a Kanani:

12. Ndipo anapereka dziko lao likhale cosiyira,Cosiyira ca kwa Israyeli anthu ace.

13. Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha;Cikumbukilo canu, Yehova, kufikira mibadwo mibadwo.

14. Pakuti Yehova adzaweruza anthu ace,Koma adzaleka atumiki ace.

15. Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golidi,Nchito ya manja a anthu.

16. Pakamwa ali napo koma osalankhula;Maso ali nao, koma osapenya;

17. Makutu ali nao, koma osamva;Inde, pakamwa pao palibe mpweya.

18. Akuwapanga adzafanana nao;Inde, onse akuwakhulupirira.

19. A nyumba ya Israyeli inu, lemekezani Yehova:A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova:

Masalmo 135