Masalmo 135:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndiye amene anapanda amitundu ambiri.Napha mafumu amphamvu;

11. Sihoni mfumu ya Aamori,Ndi Ogi mfumu ya Basana,Ndi maufumu onse a Kanani:

12. Ndipo anapereka dziko lao likhale cosiyira,Cosiyira ca kwa Israyeli anthu ace.

13. Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha;Cikumbukilo canu, Yehova, kufikira mibadwo mibadwo.

14. Pakuti Yehova adzaweruza anthu ace,Koma adzaleka atumiki ace.

15. Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golidi,Nchito ya manja a anthu.

16. Pakamwa ali napo koma osalankhula;Maso ali nao, koma osapenya;

Masalmo 135