Masalmo 135:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Haleluya;Lemekezani dzina la Yehova;Lemekezani inu atumiki a Yehova:

2. Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova,M'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.

3. Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino;Muyimbire zolemekeza dzina lace; pakuti nkokondweretsa kutero.

4. Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo,Israyeli, akhale cuma cace ceni ceni.

5. Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkuru,Ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.

Masalmo 135