6. Taonani, tinacimva m'Efrata;Tinacipeza ku cidikha ca kunkhalango.
7. Tidzalowa mokhalamo Iye;Tidzagwadira ku mpando wa mapazi ace.
8. Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;Inu ndi hema wa mphamvu yanu,
9. Ansembe anu abvale cilungamo;Ndi okondedwa anu apfuule mokondwera.
10. Cifukwa ca Davide mtumiki wanuMusabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.
11. Yehova analumbira Davide zoona;Sadzalibweza; ndi kuti,Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wacifumu wako.