3. Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga,Ngati ndidzakwera pa kama logonapo;
4. Ngati ndidzalola maso anga agone,Kapena zikope zanga ziodzere;
5. Kufikira nditapezera Yehova malo,Cokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?
6. Taonani, tinacimva m'Efrata;Tinacipeza ku cidikha ca kunkhalango.
7. Tidzalowa mokhalamo Iye;Tidzagwadira ku mpando wa mapazi ace.
8. Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;Inu ndi hema wa mphamvu yanu,
9. Ansembe anu abvale cilungamo;Ndi okondedwa anu apfuule mokondwera.