Masalmo 132:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga,Ngati ndidzakwera pa kama logonapo;

4. Ngati ndidzalola maso anga agone,Kapena zikope zanga ziodzere;

5. Kufikira nditapezera Yehova malo,Cokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?

6. Taonani, tinacimva m'Efrata;Tinacipeza ku cidikha ca kunkhalango.

7. Tidzalowa mokhalamo Iye;Tidzagwadira ku mpando wa mapazi ace.

8. Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;Inu ndi hema wa mphamvu yanu,

Masalmo 132