4. Akadatimiza madziwo,Mtsinje ukadapita pa moyo wathu;
5. Madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu.
6. Alemekezedwe Yehova,Amene sanatipereka kumano kwao tikhale cakudya cao.
7. Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi;Msampha unatyoka ndi ife tinaonioka.
8. Thandizo lathu liri m'dzina la Yehova,Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.