Masalmo 12:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;Pakuti okhulupirika acepa mwa ana a anthu.

2. Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wace:Amanena ndi mlomo wotyasika, ndi mitima iwiri.

3. Yehova adzadula milomo yonse yotyasika,Lilime lakudzitamandira:

4. Amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;Milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?

Masalmo 12