68. Inu ndinu wabwino, ndi wakucita zabwino;Mundiphunzitse malemba anu.
69. Odzikuza anandipangira bodza:Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
70. Mtima wao unona ngati mafuta;Koma ine ndikondwera naco cilamulo canu.
71. Kundikomera kuti ndinazunzidwa;Kuti ndiphunzire malemba anu.
72. Cilamulo ca pakamwa panu cindikomeraKoposa golidi ndi siliva zikwi zikwi.
73. Manja anu anandilenga nandiumba;Mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.