54. Malemba anu anakhala nyimbo zangaM'nyumba ya ulendo wanga,
55. Usiku ndinakumbukila dzina lanu, Yehova,Ndipo ndinasamalira cilamulo canu.
56. Ici ndinali naco,Popeza ndinasunga malangizo anu.
57. Yehova ndiye gawo langa:Ndinati ndidzasunga mau anu.
58. Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse:Mundicitire cifundo monga mwa mau anu.
59. Ndinaganizira njira zanga,Ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.
60. Ndinafulumira, osacedwa,Kusamalira malamulo anu.
61. Anandikulunga nazo zingwe za oipa;Koma sindinaiwala cilamulo canu.
62. Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikaniCifukwa ca maweruzo anu olungama.