Masalmo 119:38-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Limbitsirani mtumiki wanu mau anu,Ndiye wodzipereka kukuopani.

39. Mundipatutsire cotonza canga ndiciopaco;Popeza maweruzo anu ndi okoma.

40. Taonani, ndinalira malangizo anu;Mundipatse moyo mwa cilungamo canu.

41. Ndipo cifundo canu cindidzere, Yehova,Ndi cipulumutso canu, monga mwa mau anu.

42. Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;Popeza ndikhulupirira mau anu.

43. Ndipo musandicotsere ndithu mau a coonadi pakamwa panga;Pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.

44. Potero ndidzasamalira malamulo anu cisamalireKu nthawi za nthawi.

45. Ndipo ndidzayenda mwaufulu;Popeza ndinafuna malangizo anu.

46. Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu,Osacitapo manyazi.

Masalmo 119