Masalmo 119:15-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndidzalingirira pa malangizo anu,Ndi kupenyerera mayendedwe anu.

16. Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu;Sindidzaiwala mau anu,

17. Mucitire cokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo;Ndipo ndidzasamalira mau anu.

18. Munditsegulire maso, kuti ndipenyeZodabwiza za m'cilamulo canu.

19. Ine ndine mlendo pa dziko lapansi;Musandibisire malamulo anu.

20. Mtima wanga wasweka ndi kukhumbaMaweruzo anu nyengo zonse.

21. Munadzudzula odzikuza otembereredwa,Iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.

22. Mundicotsere cotonza, ndi cimpepulo;Pakuti ndinasunga mboni zanu.

23. Nduna zomwe zinakhala zondineneza;Koma mtumiki wanu analingirira malemba anu.

24. Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa,Ndizo zondipangira nzeru.

Masalmo 119