Masalmo 119:127-131 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

127. Cifukwa cace ndikonda malamulo anuKoposa golidi, Inde golidi woyengeka,

128. Cifukwa cace ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse;Koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.

129. Mboni zanu nzodabwiza; Cifukwa cace moyo wanga uzisunga,

130. Potsegulira mau anu paunikira;Kuzindikiritsa opusa.

131. Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefu wefu;Popeza ndinakhumba malamulo anu.

Masalmo 119