Masalmo 119:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Inu ndinu wodala Yehova;Ndiphunzitseni malemba anu.

13. Ndinafotokozera ndi milomo yangaMaweruzo onse a pakamwa panu,

14. Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu,Koposa ndi cuma conse,

15. Ndidzalingirira pa malangizo anu,Ndi kupenyerera mayendedwe anu.

16. Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu;Sindidzaiwala mau anu,

17. Mucitire cokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo;Ndipo ndidzasamalira mau anu.

18. Munditsegulire maso, kuti ndipenyeZodabwiza za m'cilamulo canu.

19. Ine ndine mlendo pa dziko lapansi;Musandibisire malamulo anu.

Masalmo 119