12. Adandizinga ngati njuci;Anazima ngati moto waminga;Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
13. Kundikankha anandikankha ndikadagwa;Koma Yehova anandithandiza.
14. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;Ndipo anakhala cipulumutso canga.
15. M'mahema a olungama muli liu lakupfuula mokondwera ndi la cipulumutso:
16. Dzanja lamanja la Yehova licita mwamphamvu.