Masalmo 118:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Amitundu onse adandizinga,Zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.

11. Adandizinga, inde, adandizinga:Indedi, m'dzinala Yehova ndidzawaduladula.

12. Adandizinga ngati njuci;Anazima ngati moto waminga;Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.

13. Kundikankha anandikankha ndikadagwa;Koma Yehova anandithandiza.

14. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;Ndipo anakhala cipulumutso canga.

Masalmo 118