6. Yehova asunga opusa;Ndidafoka ine, koma anandipulumutsa,
7. Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako;Pakuti Yehova anakucitira cokoma.
8. Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa,Maso anga kumisozi, Mapazi anga, ndingagwe.
9. Ndidzayenda pamaso pa Yehova M'dziko la amoyo.
10. Ndinakhulupirira, cifukwa cace ndinalankhula;Ndinazunzika kwambiri.
11. Pofulumizidwa mtima ndinati ine,Anthu Onse nga mabodza.
12. Ndidzabwezera Yehova cianiCifukwa ca zokoma zace zonse anandicitira?
13. Ndidzanyamula cikho ca cipulumutso,Ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova,