Masalmo 116:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Imfa ya okondedwa aceNja mtengo wace pamaso pa Yehova.

16. Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu;Ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;Mwandimasulira zondimanga,

17. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yaciyamiko,Ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.

18. Ndidzacita zowinda zanga za kwa Yehova,Tsopano, pamaso pa anthu ace onse;

19. M'mabwalo a nyumba ya Yehova,Pakati pa inu, Yerusalemu. Haleluya.

Masalmo 116