2. Pakuti, onani, oipa akoka uta,Apiringidza mubvi wao pansinga,Kuwaponyera mumdima oongoka mtima.
3. Akapasuka maziko,Wolungama angacitenji?
4. Yehova ali m'Kacisi wace woyera,Yehova, mpando wacifumu wace uli m'Mwamba;Apenyerera ndi maso ace, ayesa ana a anthu ndi zikope zace.
5. Yehova ayesa wolungama mtima:Koma moyo wace umuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa.