Masalmo 107:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Anasokera m'cipululu, m'njira yopanda anthu;Osapeza mudzi wokhalamo.

5. Anamva njala ndi ludzu,Moyo wao unakomoka m'kati mwao.

6. Pamenepo anapfuulira kwa Yehova mumsauko mwao,Ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao.

7. Ndipo anawatsogolera pa njira yolunjika,Kuti amuke ku mudzi wokhalamo.

8. Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!

Masalmo 107