Masalmo 107:16-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Popeza adaswa zitseko zamkuwa,Natyola mipiringidzo yacitsulo.

17. Anthu opusa azunzika cifukwa ca zolakwa zao,Ndi cifukwa ca mphulupulu zao.

18. Mtima wao unyansidwa naco cakudya ciri conse;Ndipo ayandikira zipata za imfa.

19. Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao.

Masalmo 107