14. Anawaturutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,Nadula zomangira zao.
15. Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
16. Popeza adaswa zitseko zamkuwa,Natyola mipiringidzo yacitsulo.
17. Anthu opusa azunzika cifukwa ca zolakwa zao,Ndi cifukwa ca mphulupulu zao.
18. Mtima wao unyansidwa naco cakudya ciri conse;Ndipo ayandikira zipata za imfa.
19. Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao.
20. Atumiza mau ace nawaciritsa,Nawapulumutsa ku cionongeko cao.