Masalmo 106:21-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Anaiwala Mulungu mpulumutsi wao,Amene anacita zazikulu m'Aigupto;

22. Zodabwiza m'dziko la Hamu,Zoopsa ku Nyanja Yofiira.

23. Potero Iye adati awaononge,Pakadapanda Mose wosankhika wace, kuima pamaso pace pagamukapo,Kubweza ukali wace ungawaononge,

24. Anapeputsanso dziko lofunika,Osabvomereza mau ace;

25. Koma anadandaula m'mahema mwao,Osamvera mau a Yehova.

26. Potero anawasamulira dzanja lace,Kuti awagwetse m'cipululu:

Masalmo 106