11. Ndipo madziwo anamiza owasautsa;Sanatsala mmodzi yense.
12. Pamenepo anabvomereza mau ace;Anayimbira comlemekeza.
13. Koma anaiwala nchito zace msanga;Sanalindira uphungu wace:
14. Popeza analaka-lakatu kucidikhako,Nayesa Mulungu m'cipululu.
15. Ndipo anawapatsa copempha iwo;Koma anaondetsa mitima yao.
16. Ndipo kumisasa anacita nao nsanje MoseNdi Aroni woyerayo wa Yehova.
17. Dziko lidayasama nilidameza Datani,Ndipo linafotsera gulu la Abiramu.
18. Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto;Lawi lace lidapsereza oipawo.