Masalmo 105:17-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Anawatsogozeratu munthu;Anamgulitsa Yosefe akhale kapolo:

18. Anapweteka miyendo yace ndi matangadza;Anamgoneka m'unyolo;

19. Kufikira nyengo yakucitika maneno ace;Mau a Yehova anamuyesa.

20. Mfumuyo anatuma munthu nammasula;Woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira.

21. Anamuika akhale woyang'anira nyumba yace,Ndi woweruza wa pa zace zonse:

22. Amange nduna zace iye mwini,Alangize akulu ace adziwe nzeru.

23. Pamenepo Israyeli analowa m'Aigupto;Ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu.

24. Ndipo anacurukitsatu mtundu wa anthu ace,Nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa.

Masalmo 105