1. Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita Iye.
2. Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.
3. Mudzitamandire ndi dzina lace loyera:Mitima yao ya iwo ofunsira Yehova ikondwere.
4. Funani Yehova, ndi mphamvu yace;Funsirani nkhope yace nthawi zonse.
5. Kumbukilani zodabwiza zace adazicita;Zizindikilo zace ndi maweruzo a pakamwa pace;