Masalmo 103:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino;Nabweza ubwana wako unge mphungu.

6. Yehova acitira onse osautsidwa Cilungamo ndi ciweruzo.

7. Analangiza Mose njira zace,Ndi ana a Israyeli macitidwe ace.

8. Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wacisomo,Wosakwiya msanga, ndi wa cifundo cocuruka.

9. Sadzatsutsana nao nthawi zanse;Ndipo sadzasunga mkwiyo wace kosatha.

10. Sanaticitira monga mwa zolakwa zathu,Kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.

Masalmo 103