Masalmo 103:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Amene akhululukira mphulupulu zako zonse;Naciritsa nthenda zako zonse;

4. Amene aombola moyo wako ungaonongeke;Nakubveka korona wa cifundo ndi nsoni zokoma:

5. Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino;Nabweza ubwana wako unge mphungu.

6. Yehova acitira onse osautsidwa Cilungamo ndi ciweruzo.

7. Analangiza Mose njira zace,Ndi ana a Israyeli macitidwe ace.

8. Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wacisomo,Wosakwiya msanga, ndi wa cifundo cocuruka.

Masalmo 103