5. Wakuneneza mnzace m'tseri ndidzamdula;Wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
6. Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine;Iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.
7. Wakucita cinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga;Wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.