Masalmo 10:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. M'kamwa mwace mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kucenjerera;Pansi pa lilime lace pali cibvutitso copanda pace.

8. Akhala m'molalira midzi;Mobisalamo akupha munthu wosacimwa:Ambisira waumphawi nkhope yace,

9. Alalira monga mkango m'ngaka mwace;Alalira kugwira wozunzika:Agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwace.

10. Aunthama, nawerama,Ndipo aumphawi agwa m'zala zace.

11. Anena m'mtima mwace, Mulungu waiwala;Wabisa nkhope yace; sapenya nthawi zonse,

12. Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;Musaiwale ozunzika.

13. Woipa anyozeranii Mulungu,Anena m'mtima mwace, Simudzafunsira?

Masalmo 10