Marko 2:26-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Kuti, analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?

27. Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa cifukwa ca munthu, si munthu cifukwa ca Sabata;

28. motero Mwana wa munthu ali mwini dzuwa la Sabata lomwe.

Marko 2