Marko 2:23-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda dzuwa la Sabata; ndipo ophunzira ace poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu.

24. Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, acitiranji cosaloleka kucitika dzuwa la Sabata?

25. Ndipo ananena nao, Simunawerenga konse cimene anacicita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye?

26. Kuti, analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?

27. Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa cifukwa ca munthu, si munthu cifukwa ca Sabata;

28. motero Mwana wa munthu ali mwini dzuwa la Sabata lomwe.

Marko 2