Marko 13:28-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo phunzirani ndi mkuyu fanizo lace; pamene pafika kuti nthambi yace ikhala yanthete, ndipo anaphuka masamba ace, muzindikira kuti layandikira dzinja;

29. comweco inunso, pamene muona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti ali pafupi pakhomo.

30. Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitacitika.

31. Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.

32. Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yace sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.

33. Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yace.

Marko 13