1. Ndipo pamene analikuturuka Iye m'Kacisi, mmodzi wa ophunzira ace ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.
2. Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikuru? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzace, umene sudzagwetsedwa.
3. Ndipo pamene anakhala Iye pa phiri la Azitona, popenyana ndi Kacisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andreya, kuti,
4. Tiuzeni, zinthu izi zidzacitika liti? Ndi cotani cizindikilo cace cakuti ziri pafupi pa kumarizidwa zinthu izi zonse?
5. Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusoceretseni.
6. Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasoceretsa ambiri.