30. ndipouzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.
31. Laciwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.
32. Ndipo mlembiyo anati kwa Iye, Cabwino, Mphunzitsi, mwanena zoona kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye:
33. ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzace monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.