30. Ubatizo wa Yohane ucokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? Mundiyankhe.
31. Ndipo anatsutsana mwa iwo okha, nanena, Tikati, Kumwamba; adzanena iye, Ndipo simunakhulupirira iye bwanji?
32. Koma tikati, Kwa anthu —anaopa anthuwo; pakuti onse anamuyesa Yohane mneneri ndithu.
33. Ndipo iwo anamyankha Yesu, nanena, Sitidziwa. Ndipo Yesu ananena nao, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu zimenezi.