Marko 1:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo anakhala m'cipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zirombo, ndipo angelo anamtumikira.

14. Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira uthenga wabwino wa Mulungu,

15. nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.

16. Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andreya, mbale wace wa Simoni, alinkuponya psasa m'nyanja; pakuti anali asodzi.

17. Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.

18. Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye.

Marko 1