Maliro 5:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Anyamata ananyamula mphero,Ana nakhumudwa posenza nkhuni.

14. Akulu adatha kuzipata,Anyamata naleka nyimbo zao.

15. Cimwemwe ca mtima wathu calekeka,Masewera athu asanduka maliro.

16. Korona wagwa pamutu pathu;Kalanga ife! pakuti tinacimwa.

17. Cifukwa ca ici mtima wathu ufoka,Cifukwa ca izi maso athu acita cimbuuzi;

18. Pa phiri la Ziyoni lopasukaloAnkhandwe ayendapo.

Maliro 5