10. Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;Aponya pfumbi pa mitu yao, namangirira ciguduli m'cuuno mwao:Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.
11. Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka;Ciwindi canga cagwa pansi cifukwa ca kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga;Cifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.
12. Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu,Potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.
13. Ndikucitire umboni wotani? ndikuyerekeze ndi ciani, mwana wamkazi wa Yerusalemu?Ndikulinganize ndi ciani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?Popeza akula ngati nyanja; ndani angakucize?