Malaki 4:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akucita coipa, adzakhala ngati ciputu; ndi tsiku lirinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.

2. Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la cilungamo lidzakuturukirani, muli kuciritsa m'mapiko mwace; ndipo mudzaturuka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng'ombe onenepa,

3. Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa ku mapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wamakamu.

4. Kumbukilani cilamulo ca Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliraco m'Horebu cikhale ca Israyeli lonse, ndico malemba ndi maweruzo.

Malaki 4